Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphatso Yaulere
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Mphatso Yaulere oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri!
Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu, bwerani madzi alipo; ndipo inu amene mulibe ndalama bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye! Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Pakuti ngati, chifukwa cha kulakwa kwa munthu mmodziyo, imfa inalamulira kudzera mwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga kwa iwo amene adzalandira chisomo chochuluka ndi mphatso yachilungamo, adzalamulira mʼmoyo kudzera mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu.
Choncho monga tchimo limodzi linabweretsa kutsutsika pa anthu onse, chimodzimodzinso ntchito imodzi yolungama inabweretsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo.
Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.
ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.
Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama!
Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa.