Mavesi a m'Baibulo Onena za Phindu Loona Mtima
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Phindu Loona Mtima oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.
Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.
“ ‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu. Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto.
Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.
Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire. Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera, ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
“ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake. “ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.