Mavesi a m'Baibulo Onena za Pezani Nzeru

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Pezani Nzeru oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 4:7

Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.

02 Miyambo 3:13-14

Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.

03 Miyambo 16:16

Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

04 Miyambo 8:11

Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.

05 Miyambo 23:23

Gula choonadi ndipo usachigulitse; ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.

06 Miyambo 2:1-5

Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako, ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu; ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu, ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika, ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.

07 Miyambo 19:8

Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

Mitu yofanana