Mavesi a m'Baibulo Onena za Mgonero

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mgonero oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.

02 1 Yohane 1:7

Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

03 Ahebri 10:24-25

Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.

05 Afilipi 2:1-2

Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso.

06 1 Yohane 1:3

Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu.

07 1 Akorinto 1:9

Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.

Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake.

Mitu yofanana