Mavesi a m'Baibulo Onena za Kubweretsa Mtendere

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kubweretsa Mtendere oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 5:9

Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

02 Aroma 12:18

Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere.

03 Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.

04 Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.

05 Yakobo 3:18

Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.

Mitu yofanana