Mavesi a m'Baibulo Onena za Thupi la Khristu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Thupi la Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Akorinto 12:27

Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.

02 1 Akorinto 12:12

Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.

03 Aroma 12:4-5

Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.

04 Aefeso 4:15-16

Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo. Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.

05 1 Akorinto 12:18

Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira.

06 1 Akorinto 12:14

Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.

Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha. Diso silingawuze dzanja kuti, “Iwe sindikukufuna!” Ndipo mutu sungawuze phazi kuti “Iwe sindikukufuna!”

08 Aefeso 4:16

Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.

09 1 Akorinto 12:25

kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane.

10 Aroma 12:6

Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.

11 Akolose 1:18

Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse.

Mitu yofanana