Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusenzerana Mitolo

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kusenzerana Mitolo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Agalatiya 6:2

Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.

02 Aroma 15:1

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha.

03 1 Akorinto 12:26

Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

04 Aroma 12:15

Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.

05 Akolose 3:13

Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.

06 Agalatiya 6:9-10

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

07 1 Atesalonika 5:14

Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense.

Mitu yofanana