Mavesi a m'Baibulo Onena za Ubwenzi
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Ubwenzi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.
Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu: Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino, koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.
Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani.
Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru; koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake ndi kukodwa mu msampha.
Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.”