Mavesi a m'Baibulo Onena za Ovala Kudzichepetsa

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Ovala Kudzichepetsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 5:5

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

02 Akolose 3:12

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.

03 1 Petro 5:6

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.

04 Afilipi 2:3

Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.

05 Miyambo 11:2

Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

06 Yakobo 4:6

Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Mitu yofanana