Mavesi a m'Baibulo Onena za Abba, Atate

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Abba, Atate oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 8:15

Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.”

02 Agalatiya 4:6

Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”

03 Marko 14:36

Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”

04 Aroma 8:16

Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.

05 Mateyu 6:9

“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe,

06 Yohane 20:17

Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”

07 Agalatiya 4:7

Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.

08 Aefeso 2:18

Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

09 1 Yohane 3:1

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

10 Yohane 1:12

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

11 Ahebri 4:16

Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

Mitu yofanana