Mavesi a m'Baibulo Onena za Moto Wonyeketsa
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Moto Wonyeketsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.
Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.
Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo.
Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa.
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha; anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera: Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa? Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.
Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.
ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.
Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake.