Mavesi a m'Baibulo Onena za Chinsinsi cha Uthenga Wabwino

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Chinsinsi cha Uthenga Wabwino oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Akolose 1:26

chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima.

02 Akolose 1:27

Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.

03 Aefeso 3:6

Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.

04 Aefeso 1:9

Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake.

05 1 Timoteyo 3:16

Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.

06 Aefeso 3:9

Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse.

07 1 Akorinto 2:7

Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi.

Mitu yofanana