Mavesi a m'Baibulo Onena za Ufumu wa Mulungu
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Ufumu wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.
“Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”
“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.
Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu.
“Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.