Mavesi a m'Baibulo Onena za Tsiku la Chiweruzo
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Tsiku la Chiweruzo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.
Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.
Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula.
Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”
“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi.