Mavesi a m'Baibulo Onena za Palibenso Misozi

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Palibenso Misozi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Chivumbulutso 21:4

‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

02 Yesaya 25:8

Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.

03 Chivumbulutso 7:17

Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

04 Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.

05 Masalimo 126:5

Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

07 Yesaya 60:20

Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzazimiriranso; Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya, ndipo masiku a mavuto ako adzatha.

08 Yeremiya 31:13

Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala. Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala. Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo; ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.

09 Mateyu 5:4

Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.

Mitu yofanana