Mavesi a m'Baibulo Onena za Machimo Osakumbukirikanso
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Machimo Osakumbukirikanso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
“Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini, ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake, kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’ chifukwa onse adzandidziwa Ine, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,” akutero Yehova. “Ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
Ndipo akutinso: “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi zolakwa zawo.”
Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere kuti ndikhale ndi moyo; Inu munandisunga kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko chifukwa mwakhululukira machimo anga onse.
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
Ngodala munthu amene machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”