Mavesi a m'Baibulo Onena za Kutembenukira kwa Mulungu
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kutembenukira kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,
Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
“Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”
Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako. Machimo anu ndi amene akugwetsani! Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.
kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona.
Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.
Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.