Mavesi a m'Baibulo Onena za Chisoni Chauzimu
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Chisoni Chauzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.
Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.
Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
“Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’
Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.
Ndikuvomereza mphulupulu zanga; ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija. Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”
“Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.
Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri.
Popeza tatembenuka mtima, ndiye tikumva chisoni; popeza tazindikira ndiye tikudziguguda pachifukwa. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’