Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhululukiro cha Machimo
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Chikhululukiro cha Machimo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.
Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu
Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”
Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika. Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.
Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.
Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
“Odala ndi amene zoyipa zawo zakhululukidwa; amene machimo awo afafanizidwa. Ngodala munthu amene machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”
Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.
Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo.
Ndipo akutinso: “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi zolakwa zawo.” Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.