Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulamulira Pamodzi ndi Khristu

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kulamulira Pamodzi ndi Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Timoteyo 2:12

Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

02 Chivumbulutso 22:5

Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

03 Chivumbulutso 5:10

Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.”

04 Aroma 8:17

Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

05 Chivumbulutso 3:21

Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.

06 Chivumbulutso 20:6

Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.

07 Danieli 7:18

Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’

Mitu yofanana