Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Weniweni ndi Munthu Weniweni
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Mulungu Weniweni ndi Munthu Weniweni oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu.
Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.
Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu.
Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.
Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.
pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”
Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.
Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.