Mavesi a m'Baibulo Onena za Mwana wa Mulungu

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mwana wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 20:31

Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

02 Mateyu 3:17

Ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa amene ndikondwera naye.”

03 Mateyu 16:16

Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”

04 Aroma 1:4

Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu,

05 1 Yohane 5:11-12

Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

06 Ahebri 1:5

Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”

07 Yohane 3:16

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

08 Marko 1:1

Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,

09 Luka 1:35

Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.

10 Yohane 5:25

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.

11 Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

12 Yohane 10:36

nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’

Mitu yofanana