Mavesi a m'Baibulo Onena za Muyaya Pamodzi ndi Ambuye
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Muyaya Pamodzi ndi Ambuye oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.
Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.
“Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.
Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.
Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.
Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse; mumandigwira dzanja langa lamanja. Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye.
Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri.
Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.