Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuwala kwa Dziko
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Kuwala kwa Dziko oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
Mwa Iye munali moyo, ndipo moyowo unali kuwunika kwa anthu. Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire.
Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.
Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.
Anthu oyenda mu mdima awona kuwala kwakukulu; kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani kuwunika kwawafikira.
Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”