Mavesi a m'Baibulo Onena za Bwererani kwa Yehova

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Bwererani kwa Yehova oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Hoseya 6:1

“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.

02 Yoweli 2:13

Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.

03 Malaki 3:7

Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’

04 Zekariya 1:3

Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

05 Yesaya 55:7

Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.

06 Maliro 3:40

Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu, ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.

07 Yeremiya 3:22

Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika; ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.” “Inde, tidzabwerera kwa Inu pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.

Mitu yofanana