Mavesi a m'Baibulo Onena za Konda Mnansi Wako

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Konda Mnansi Wako oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Marko 12:31

Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”

02 Levitiko 19:18

“ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.

03 Luka 10:27

Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”

04 Agalatiya 5:14

Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”

05 Aroma 13:9-10

Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

06 Mateyu 22:39

Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’

07 Yakobo 2:8

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino.

08 Aroma 15:2

Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa.

09 Luka 10:36-37

“Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?” Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.” Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”

10 Mateyu 7:12

Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.

Mitu yofanana