Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikondi Sichilephera
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Chikondi Sichilephera oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.
Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu.
Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga?
Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.
Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.