Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikondi
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Chikondi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.
Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.
Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.
Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu.
Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.