Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukonda Adani
Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kukonda Adani oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
01 Mateyu 5:44
Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani
02 Luka 6:27-28
“Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.
03 Aroma 12:20
Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”
Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
05 Aroma 12:14
Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere.