Mavesi a m'Baibulo Onena za Wobisika ndi Khristu
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Wobisika ndi Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.
Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela
Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga.
Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.
Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa, kuwateteza ku ziwembu za anthu; mʼmalo anu okhalamo mumawateteza kwa anthu owatsutsa.
Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa, anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake; Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa ndipo anandibisa mʼchimake.