Mavesi a m'Baibulo Onena za Mpesa ndi Nthambi
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Mpesa ndi Nthambi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda.
Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri.
Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa.
Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu.
Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.
Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.
Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto; munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo. Munawulimira munda wamphesawo, ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye. Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Ngati nthambi zina zinakhadzulidwa ndipo inu, inu ndiye nthambi za olivi wakuthengo, nʼkulumikizidwa pamalo pa nthambi zimenezo, ndipo tsopano mukulandira nawo zakudya zochokera ku mizu ya olivi,
Ndidzamuyimbira bwenzi langa nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa: Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde. Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.