Mavesi a m'Baibulo Onena za Koposa Zonse, Valani Chikondi
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Koposa Zonse, Valani Chikondi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
01 Akolose 3:14
Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
03 Akolose 3:12
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
04 1 Petro 4:8
Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.
05 Aroma 13:8
Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.
Chitani zonse mwachikondi.