Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuuka kwa Akufa ndi Kupambana Imfa
Khristu wauka — manda ali opanda kanthu ndipo imfa yagonjetsedwa. Chifukwa Iye ali ndi moyo, iwo ophatikizidwa naye akuukitsidwa ku moyo watsopano ndi kupatsidwa chiyembekezo chamoyo. Mavesi awa amakondwerera kuuka ndi chigonjetso chimene ndi chathu mwa Iye.
Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo.
Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”
Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe.
Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.
Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka.
Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake
Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.
Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo.