Mavesi a m'Baibulo Onena za Zipatso Zoyamba

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Zipatso Zoyamba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Akorinto 15:23

Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka.

02 1 Akorinto 15:20

Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo.

03 Aroma 8:11

Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.

04 Akolose 1:18

Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse.

05 1 Atesalonika 4:14

Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.

06 1 Akorinto 15:22

Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo.

Iwo ananena kuti Khristu adzamva zowawa ndipo popeza Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalalikira za kuwunika kwa anthu a mtundu wake ndiponso kwa anthu a mitundu ina.”

08 Chivumbulutso 1:5

ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake,

09 Yakobo 1:18

Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.

10 Aroma 8:23

Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.

11 1 Petro 1:3

Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa,

12 Yohane 12:24

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’

13 1 Akorinto 15:21

Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu.

14 Akolose 1:15

Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse.

15 Chivumbulutso 1:18

Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.

Mitu yofanana