Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuuka kwa Akufa ndi Moyo

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kuuka kwa Akufa ndi Moyo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 11:25

Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo.

02 Yohane 11:26

Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”

03 Yohane 5:24

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.

04 Yohane 6:40

Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”

05 1 Akorinto 15:22

Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo.

Mitu yofanana