Mavesi a m'Baibulo Onena za Njira, Choonadi ndi Moyo

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Njira, Choonadi ndi Moyo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 14:6

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

02 Yohane 10:9

Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

04 Yohane 11:25

Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo.

05 Ahebri 10:20

Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.

06 Yohane 1:17

Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu.

07 Yohane 8:32

Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

08 Ahebri 10:19-20

Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.

09 Yohane 6:68

Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.

10 Aefeso 2:18

Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

11 1 Yohane 5:20

Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.

Mitu yofanana