Mavesi a m'Baibulo Onena za Wokwanira mwa Khristu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Wokwanira mwa Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Akolose 2:10

Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse.

02 Akolose 2:9

Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu.

03 2 Petro 1:3

Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake.

04 Aefeso 3:19

Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.

05 Ahebri 10:14

Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

06 Akolose 1:28

Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu.

07 Afilipi 1:6

Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

08 Ahebri 13:21

akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni.

09 1 Akorinto 1:30

Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.

10 Aefeso 1:3

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.

11 Ahebri 12:2

Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.

12 Afilipi 4:19

Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

13 Akolose 2:6-7

Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.

14 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.

Mitu yofanana