Yobu 25
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Biblica)
Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
“Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.
Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?
Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?
Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,
nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”
Yobu
Tsegulani chowerengera chogwirizana kusintha matembenuzidwe, kusintha malembedwe, ndi kulemba zizindikiro pa mavesi — kapena onani mavesi malinga ndi mutu.
© 2002, 2016 Biblica, Inc. · CC BY-SA 4.0